info@exploitsonline.com  |  +265 998 955 220
VLE Portal  |  Main Website
Menu
Home About News Programmes Campuses Mode of Delivery
VLE Portal Apply Now

Alumni Testimony on Exploits University Bob Emmanuel Chisamba

Alumni Testimony on Exploits University Bob Emmanuel Chisamba

Alumni Testimony on Exploits University Bob Emmanuel Chisamba

Makolo ngati ndalama zilipo, ana apititseni ku private universities omwe ali accredited, osagwa ulesi. Bwanawa pano ali ndi ma masters awiri, ina ya distinction, onse anawapeza pa scholarship koma anapita ku private university komwe anakapanga first degree yake ndikukhozaso ndi distinction.

Iyeyu, Bob Emmanuel Chisamba, tinali limodzi ku Maranatha private schools, ku Madisi, Dowa. Ndipo anakhoza 17 points  kenaka anakapanga degree ya accounting ku Exploits University ndikukhoza ndi distinction.

Mu 2020 analandila scholarship kuchokera ku Government of India kukapanga Masters ya Business Administration in Finance.

Mu 2022, anapita ku UK kukapanga Masters in Global Central Banking and Financial Regulation ndipo anakakhozako ndi distinction kumeneko. Inali Commonwealth scholarship imeneyi.

Bob anasankhidwa ngati president wa Malawi Red Cross Society - Youth Arm komaso Board member wa Red Cross. Mu 2024, anasankhidwa kukhala Global Youth Commissioner wa International Federation of Red Cross and Red Crescent Societies (IFRC).

Anapitakoso ku USA ngati fellow Ku university ya The State University of New Jersey mu nchaka cha 2022.

Wagwirapo ntchito ndina Company osiyanasiyana monga MasterCard Foundation, Restless Development Uganda, RTU International komaso GIZ Malawi ndipo pano ndi Assistant Manager- Grant and Finance ku Family Health Services yomwe kale inkadziwika kuti PSI Malawi.

Bob Chisamba aliso ndi multimillion company yotchedwa InteWaste yomwe ili mu Lilongwe umu yomwe imapanga za wastes management. By the way, Bob ali ndi zaka 30. 

So, uthenga wanga ndiwakuti, ma university or ma college omwe si aboma, akhulupilireni ndithu ngati ali accredited ndipo ngati ka khobidi kalipo, ndipo mwana amusiya za NCHE, osagwera ulesi, apite kuma private universities and colleges omwe ali ovomelezeka ndi NCHE akapange degree yomwe akufuna. Ndizotheka.

Ready to Join Exploits University?

Apply online today and take the first step towards a brighter future.

Apply Now